Proverbs 22

1Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri;
kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide.

2Wolemera ndi wosauka ndi ofanana;
onsewa anawalenga ndi Yehova.

3Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.

4Mphotho ya munthu wodzichepetsa
ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.

5Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha,
koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.

6Mwana muzimuphunzitsa njira yake,
ndipo akadzakalamba sadzachokamo.

7Wolemera amalamulira wosauka,
ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.

8Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto,
ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka.

9Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika,
pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

10Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha;
mapokoso ndi zonyoza zidzaleka.

11Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino,
adzakhala bwenzi la mfumu.

12Maso a Yehova amakhala pa anthu odziwa bwino zinthu,
koma Iye adzalepheretsa mawu a anthu osakhulupirika.

13Munthu waulesi amati,
“Kunjaku kuli mkango. Ine ndidzaphedwa mʼmisewu!”

14Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama;
amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.

15Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana,
koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

16Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake,
ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.

Malangizo a Anthu Anzeru

17Utchere khutu lako ndipo umvere mawu anzeru;
uyike mtima wako pa zimene ndikukuphunzitsa kuti udziwe.
18Zidzakhala zokondweretsa ngati uzisunga mu mtima mwako
ndi wokonzeka kuziyankhula.
19Ndakuphunzitsa zimenezi lero
koma makamaka uziopa Yehova.
20Kodi suja ndinakulembera malangizo makumi atatu
okuchenjeza ndi okupatsa nzeru,
21malangizo okudziwitsa zolungama
ndi zoona
ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?

22Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka,
ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu,
23pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo
ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.

24Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima
ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya
25kuopa kuti iwe ungadzaphunzire njira zake
ndi kukodwa mu msampha.

26Usakhale munthu wopereka chikole
kapena kukhala mboni pa ngongole;
27ngati ulephera kupeza njira yolipirira
adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.

28Usasunthe mwala wamʼmalire akalekale
amene anayikidwa ndi makolo ako.

29Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake?
Iye adzatumikira mafumu;
sadzatumikira anthu wamba.
Copyright information for NyaCCL